Numbers 7:85 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbale yasiliva iliyonse inkalemera kilogaramu limodzi ndi theka, ndipo mkhate uliwonse unkalemera magaramu 800. Siliva yense wa zipangizo zimenezo, ankalemera makilogaramu 27 ndi theka, potsata muyeso wa ku malo opatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mbale yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbale iliyonse yasiliva inkalemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndipo beseni lililonse lowazira linkalemera magalamu 800. Pamodzi, mbale zonse zasiliva zinkalemera makilogalamu 27 monga mwa muyeso wa ku malo opatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mbizi yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.