Numbers 7:88 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo nyama zonse za nsembe zachiyanjano zinali ng'ombe zamphongo 24, nkhosa zamphongo 60, atonde 60, ndi anaankhosa amphongo a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndizo zinali zopereka zopatulira guwa atalidzoza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, ana a nkhosa a caka cimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka ciperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.