Numbers 8:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisraele ndi anga, ana a anthu ndi a nyama omwe. Ndidaŵapatula onseŵa kuti akhale anga, pa tsiku limene ndidapha ana onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti a oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Aigupto, ndinadzipatulira iwo akhale anga.