Numbers 8:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aleviwo ndaŵatenga pakati pa Aisraele ndi kuŵapereka ngati mphatso kwa Aroni ndi ana ake aamuna, kuti azidzatumikira m'malo mwa Aisraele, m'chihema chamsonkhano. Azikachita mwambo wopepesera machimo a Aisraele, kuti mliri ungaŵagwere Aisraele amene ayandikire pafupi ndi malo opatulika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ake amuna yochokera mwa ana a Israele, kuchita ntchito ya ana a Israele, m'chihema chokomanako ndi kuchita chotetezera ana a Israele; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israele, pakuyandikiza ana a Israele ku malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa Aisraeli onse, ndapereka Alevi kuti akhale mphatso kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kugwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti azikapereka nsembe yopepesera machimo, kuti mliri usadzaphe Aisraeli pamene ayandikira ku malo wopatulika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ace amuna yocokera mwa ana a Israyeli, kucita nchito ya ana a Israyeli, m'cihema cokomanako ndi kucita cotetezera ana a Israyeli; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israyeli, pakuyandikiza ana a Israyeli ku malo opatulika.