Numbers 8:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi adadziyeretsa ku zoipa, ndipo adachapa zovala zao. Aroni adaŵapereka kuti akhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta, naŵachitira mwambo wopepesera machimo ao, kuti aŵayeretse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi anadziyeretsa ndi kuchapa zovala zawo. Kenaka Aaroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe yopepesera machimo yowayeretsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zobvala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawacitira cotetezera kuwayeretsa.