Numbers 8:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Alevi adapita kukagwira ntchito zao m'chihema chamsonkhano, ndipo ankatumikira Aroni ndi ana ake. Choncho Aleviwo adaŵachitira monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atatero, Alevi analowa kuchita ntchito yao m'chihema chokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawachitira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha zimenezi, Alevi anapita kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atatero, Alevi analowa kucita Debito yao m'cihema cokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ace amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawacitira.