Numbers 8:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma azithandiza abale ao m'chihema chamsonkhano ndi kumayang'anira ntchitoyo, koma asatumikire. Umu ndimo m'mene udzachitire poŵagaŵira ntchito zao Aleviwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atha kuthandiza abale awo kugwira ntchito za ku tenti ya msonkhano, koma iwowo asamagwire ntchitoyo. Mmenemu ndimo ugawire ntchito yomwe azigwira Alevi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'cihema cokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira nchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.