Numbers 9:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aisraele kuti, munthu wina aliyense mwa inu, kapena mwa zidzukulu zanu, akadziipitsa pokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala paulendo, achitebe Paska ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene wina mwa inu kapena zidzukulu zanu adetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala pa ulendo, akhoza kuchita nawo Paska ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, cifukwa ca mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azicitira Yehova Paskha.