Numbers 9:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu amene sadadziipitse ndipo sali paulendo, komabe akana kuchita Paska, ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraele, chifukwa sadabwere ndi zopereka zake kwa Chauta pa nthaŵi yake. Ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati munthu wina ali woyeretsedwa ndipo sali pa ulendo koma alephera kuchita Paska, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake chifukwa sanabweretse chopereka cha Yehova pa nthawi yake. Munthu ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kucita Paskha, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wace; popeza sanabwera naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, munthuyu asenze kucimwa kwace.