Numbers 9:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlendo akakhala pakati panu, nafuna kuchita nao Paska ya Chauta, nayenso achite Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake. Kaya ndinu alendo kapena ndinu mbadwa, nonse mukhale ndi lamulo limodzi lokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mlendo amene akukhala pakati panu, nafuna kuchita nawo Paska ya Yehova, achite nawo motsata malamulo ndi malangizo ake. Muzikhala ndi malangizo ofanana a Paska; mbadwa kapena mlendo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakacitira Yehova Paskha, azicita monga mwa lemba la Paskha, ndi monga mwa ciweruzo cace; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.