Numbers 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limene adamanga malo opatulika, mtambo udaphimba malo opatulikawo, ndiye kuti chihema chaumboni chija. Madzulo aliwonse mpaka m'maŵa mwake, mtambowo unkaphimba malo opatulika uli ndi maonekedwe a moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limene anayimika chihema, tenti ya umboni, mtambo unaphimba chihemacho. Kuyambira madzulo mpaka mmawa, mtambo umene unali pamwamba pa chihemacho unkaoneka ngati moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku loutsa kacisi mtambo unaphimba kacisi, ndiwo cihema cokomanako; ndipo madzulo padaoneka pakacisi ngati moto, kufikira m'mawa.