Numbers 9:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa Kachisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zina mtambowo unkakhala pa chihemapo masiku owerengeka. Aisraeli ankamanga misasa molamulidwa ndi Yehova ndipo ankasamukanso molamulidwa ndi Iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa kacisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'cigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.