Numbers 9:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi zina mtambowo unkangophimba chihemacho kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. M'maŵa mwake mtambowo ukachoka, iwo ankanyamuka ulendo wao. Mwina mtambowo unkaphimba chihema chija tsiku lonse ndi usiku womwe, koma ukangochokapo, iwowo ankanyamuka ulendo wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zina mtambo unkakhala kuyambira madzulo mpaka mmawa ndipo unkachoka mmawa mwake, ankasamuka. Kaya ndi masana kapena usiku, pamene mtambo wachoka, ankasamuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo; ngakhale msana ngakhale usiku, pokwera mtambo, ayenda ulendo.

Recommended Reading