Numbers 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali anthu ena amene anali atadziipitsa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kotero kuti sadathe kuchita nao Paska pa tsikulo. Motero adabwerera kwa Mose ndi kwa Aroni pa tsiku lomwelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ena a iwo sanathe kuchita nawo Paska pa tsiku limenelo chifukwa anali odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo. Choncho anabwera kwa Mose ndi Aaroni tsiku lomwelo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoza kucita Paskha tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;