Numbers 9:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adauza Mose kuti, “Ife ndife oipitsidwa chifukwa tidakhudza mtembo wa munthu. Chifukwa chiyani tikuletsedwa kubwera ndi zopereka zathu kwa Chauta pa nthaŵi yake pakati pa anzathu Aisraele?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, pakati pa ana a Israyeli?