Obadiah 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munkangoonerera pamene adani ankaŵalanda chuma chao, munkachita ngati kuvomerezana nawo, amene ankaloŵa pa zipata za Yerusalemu, namagaŵana chumacho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ake, nalowa m'zipata zake achilendo, nachitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene adani ankamulanda chuma chake pamene alendo analowa pa zipata zake ndi kuchita maere pa Yerusalemu, pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ace, nalowa m'zipata zace acilendo, nacitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.