Obadiah 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu simukadayenera kuŵanyodola abale anu Ayuda chifukwa cha tsoka lao. Simukadayenera kukondwerera kuwonongeka kwao. Simukadayenera kuŵaseka pamene iwo anali m'mavuto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wako pa nthawi ya tsoka lake, kapena kunyogodola Ayuda chifukwa cha chiwonongeko chawo, kapena kuwaseka pa nthawi ya mavuto awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka cikhakha tsiku lakupsinjika.