Obadiah 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuloŵa mu mzinda wa anthu anga. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuŵanyodola. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kulanda chuma chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu anga pa nthawi ya masautso awo, kapena kuwanyogodola pa tsiku la tsoka lawo, kapena kulanda chuma chawo pa nthawi ya masautso awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe coipa cao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao.