Obadiah 1:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simukadayenera kudikira pa mphambano za miseu kuti mugwire anthu othaŵa. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kupereka anthu ao otsala kwa adani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ake; kapena kupereka otsala ake tsiku lakupsinjika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sunayenera kudikirira pamphambano ya misewu kuti uphe Ayuda othawa, kapena kuwapereka kwa adani awo Ayuda opulumuka pa nthawi ya mavuto awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ace; kapena kupereka otsala ace tsiku lakupsinjika.