Obadiah 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu anga adamwa chikho cha zoŵaŵa pa phiri langa loyera, koma mitundu ina ya anthu idzamwa chikho cha zoŵaŵa kopitirira. Idzachita kugugudiza chikhocho kenaka nkuzimirira pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe unamwa pa phiri langa loyera, koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza; iwo adzamwa ndi kudzandira ndipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.