Obadiah 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele amene anali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanani mpaka kumpoto ku Zarefati. A ku Yerusalemu amene anali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda yakumwera ku Negebu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwera, cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli amene ali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati; a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda ya ku Negevi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo andende a khamu ili la ana a Israyeli, okhala mwa Akanani, adzakhala naco colowa cao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwela, colowa cao.