Obadiah 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwanyengedwa ndi mtima wanu wonyada. Likulu lanu lili pakati pa matanthwe, mumakhala pa mapiri aatali. Mumanena kuti, ‘Ndani angatitsitse pansi?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali, iwe amene umanena mu mtima mwako kuti, ‘Ndani anganditsitse pansi?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwace, Adzanditsitsira pansi ndani?