Obadiah 1:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu ngakhale muuluke pamwamba ngati chiwombankhanga, ngakhale mumange chisa chanu pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsanibe pansi.” Akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhanga ndi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cinkana ukwera pamwamba peni peni ngati ciombankhanga, cinkana cisanja cako cisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.