Obadiah 1:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Akuba akabwera usiku, amangotengako zimene akufuna. Okolola akamathyola zipatso, amasiyako zina. Koma inuyo adani anu akupululani kotheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu akuba akanabwera kwa iwe, kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku, aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe! Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha? Ngati anthu othyola mphesa akanafika, kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akuchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?