Philemon 1:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pano mau aŵa ndikulemba ndi dzanja langalanga kuti, “Ine Paulo ndidzalipira.” Nkosasoŵekera kukukumbutsa kuti paja iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wako womwe wachikhristuwu!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine Paulo ndicilemba ndi dzanja langa, ndidzacibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.