Philippians 1:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma oyamba aja salalika Khristu moona. Amangodzikonda okha, ndipo amafuna kundiwonjezera zoŵaŵa pamene ndili m'ndende muno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ena alalikira Khristu mochokera m'chotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m'zomangira zanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena aja amalalikira Khristu modzikonda osati moona mtima namaganiza kuti kutero kubweretsa mavuto pamene ndili mʼmaunyolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ena alalikira Kristu mocokera m'cotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira cisautso m'zomangira zanga.