Philippians 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ndikuyembekeza ndi kukhulupirira ndi mtima wonse kuti sipadzakhala konse manyazi. Koma ndikuyembekeza kuti ndidzalimba mtima kulankhula poyera, kuti tsopanonso, monga nthaŵi zonse, Khristu alemekezedwe mwa ine, ngakhale ndikhale moyo, kapena ndimwalire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndili ndi chiyembekezo chonse kuti sindidzachita manyazi ndi pangʼono pomwe, koma ndidzakhala ndi chilimbikitso chokwanira kuti monga mwa nthawi zonse, tsopano Khristu adzakwezedwa mʼthupi langa kaya ndi mʼmoyo kapena mu imfa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga mwa kulingiriritsa ndi ciyembekezo canga, kuti palibe cinthu cidzandicititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Kristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwamoyo, kapena mwa imfa.