Philippians 1:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala naco colakalaka ca kucoka kukhala ndi Kristu, ndiko kwabwino koposa-posatu;