Philippians 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuyeneradi kuganiza zotere za nonsenu, popeza kuti ndimakukondani kwambiri. Pakuti nonsenu ndinu ogwirizana nane ndithu, pamene ndili m'ndende ndiponso pamene ndikugwira ntchito iyi imene Mulungu adandipatsa mwa kukoma mtima kwake, ntchito ya kuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa ine ndi bwino kuti ndiziganiza zotere za nonsenu, popeza ndimakukondani, ngakhale ndikhale mʼndende, kapena pamene ndikuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino, inu nonse mumagawana nane chisomo cha Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndiri nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'codzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'cisomo.