Philippians 2:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati tsono muli citonthozo mwa Kristu, ngati cikhazikitso ca cikondi, ngati ciyanjano ca Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,