Philippians 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani nchito yace ya cipulumutso canu ndi mantha, ndi kunthunthumira;