Philippians 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamanga chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
akuonetsera mau a movo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira: nao m'tsiku la Kristu, kuti sindinathamanga cabe, kapena kugwiritsa nchito cabe.