Philippians 2:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa cikhulupiriro canu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;