Philippians 2:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndaganiza kuti nkofunikadi kuti ndikutumizireni mbale wathu uja, Epafrodito. Mudaamtuma kuti adzandithandize pa zosoŵa zanga, ndipo wagwiradi ntchito ndi kumenya nkhondo yachikhristu pamodzi ndi ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinayesa nkufunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinayesa nkufunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wanchito mnzanga ndi msilikari mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa cosowa canga;