Philippians 2:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamcitira cifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale naco cisoni cionjezere-onjezere.