Philippians 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini;