Philippians 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale anga, potsiriza ndikuti, “Muzikondwa mwa Ambuye.” Kukulemberaninso mau omwewo sikondilemetsa, ndipo mauwo ngokuthandizani kukhala osakayika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale anga, ndikupitiriza kunena kuti, kondwani mwa Ambuye! Sizondivuta kuti ndilembenso mawu omwewo, ndipo zimenezi nʼzokuthandizani inuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundibvuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.