Philippians 3:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimene ndikufuna nchakuti ndidziŵe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zoŵaŵa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti ndimzindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti ndimzindikire iye, ndi mphamvu ya kuuka kwace, ndi ciyanjano ca zowawa zace, pofanizidwa ndi imfa yace;