Philippians 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,