Philippians 3:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndakhala ndikukuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti monga ndakhala ndikukuwuzani kawirikawiri mʼmbuyomu, ndipo tsopano ndikunenanso ndi misozi kuti, anthu ambiri akukhala monga adani a mtanda wa Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawiri kawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Kristu;