Philippians 3:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo. Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
citsiriziro cao ndico kuonongeka, mulungu wao ndiyo niimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amenealingirira za padziko.