Philippians 3:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabeŵa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lace la ulemerero, monga mwa macitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.