Philippians 3:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabetu ineyo ndikadatha kudalira miyambo yathupiyi. Ngati alipo wina woganiza kuti ali ndi chifukwa chodalira miyambo yathupi yotere, ineyo ndili ndi chifukwa choposa apo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndingakhale inenso ndili nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ngakhale kuti ineyo ndili ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupizo. Ngati pali winanso amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupi, ineyo ndili ndi zifukwa zoposa pamenepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu;