Philippians 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu ine ndidaumbalidwa pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditabadwa. Ndine wa mtundu wa Israele, wa fuko la Benjamini, Mhebri weniweni wobadwa mwa makolo achihebri. Kunena za Malamulo achiyuda, ndinali wa gulu la Afarisi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinachita mdulidwe pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditangobadwa. Ndine wa mtundu wa Israeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, kunena za malamulo, ndinali Mfarisi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
wodulidwa tsiku lacisanu ndi citatu, wa mbadwo wa Israyeli, wa pfuko la Benjamini, Mhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;