Philippians 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kupezedwa mwa iye, wosati wakukhala naco cilungamo canga ca m'lamulo, koma cimene ca mwa cikhulupiriro ca Kristu, cilungamoco cocokera mwa Mulungu ndi cikhulupiriro;