Philippians 4:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka m'Masedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'ciyambi ca Uthenga Wabwino, pamene ndinacoka kuturuka m'Makedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a copereka ndi colandira; koma inu nokha;