Philippians 4:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndalandiradi zonse, ndipo ndili nazo zochuluka. Ndili ndi zonse zofunika tsopano, popeza kuti ndalandira kwa Epafrodito zimene mudanditumizira. Zili ngati chopereka cha fungo lokoma, ngati nsembe imene Mulungu ailandira ndi kukondwera nayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fundo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndiri nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidacokera kwanu, mnunkho wa pfungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.