Proverbs 1:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi anthu osachangamukanu, mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti? Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti? Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti? Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti? Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi mudzakonda zacibwana kufikira liti, acibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, Opusa ndi kuda nzeru?