Proverbs 10:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera, koma kwa munthu womvetsa zinthu kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masewero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa; koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa, koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa; Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.