Proverbs 11:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ungwiro wa anthu olungama umaŵatsogolera, koma makhalidwe okhota a anthu onyenga ngoononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; Koma kukhota kwa aciwembu kudzawaononga.